Ndipo m'masiku a Davide munali njala, zaka zitatu; ndipo Davide anafunsira kwa Yehova. Ndipo Yehova anati, Ndicho chifukwa cha Saulo ndi nyumba yake yamwazi, popeza iye anawapha Agibiyoni.
Masalimo 27:8 - Buku Lopatulika Pamene munati, Funani nkhope yanga; mtima wanga unati kwa Inu. Nkhope yanu, Yehova, ndidzaifuna. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamene munati, Funani nkhope yanga; mtima wanga unati kwa Inu. Nkhope yanu, Yehova, ndidzaifuna. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pajatu Inu mudati, “Muzifunafuna nkhope yanga.” Inu Chauta, ndidzafunafuna nkhope yanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtima wanga ukuti kwa Inu, “Funafuna nkhope yake!” Nkhope yanu Yehova ndidzayifunafuna. |
Ndipo m'masiku a Davide munali njala, zaka zitatu; ndipo Davide anafunsira kwa Yehova. Ndipo Yehova anati, Ndicho chifukwa cha Saulo ndi nyumba yake yamwazi, popeza iye anawapha Agibiyoni.
ndipo anthu anga otchedwa dzina langa akadzichepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zao zoipa; pamenepo ndidzamvera mu Mwamba, ndi kukhululukira choipa chao, ndi kuchiritsa dziko lao.
Ndinapemba pankhope panu ndi mtima wanga wonse: Mundichitire chifundo monga mwa mau anu.
Ine sindinanene m'tseri m'malo a dziko la mdima; Ine sindinati kwa mbeu ya Yakobo, Mundifune Ine mwachabe; Ine Yehova ndinena chilungamo, ndinena zimene zili zoona.
Ndidzamuka ndi kubwerera kunka kumalo kwanga, mpaka adzavomereza kupalamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwachangu.