Masalimo 27:7 - Buku Lopatulika Imvani, Yehova, liu langa pofuula ine; mundichitirenso chifundo ndipo mundivomereze. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Imvani, Yehova, liu langa pofuula ine; mundichitirenso chifundo ndipo mundivomereze. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Imvani, Inu Chauta, pamene ndikulira mofuula, mundikomere mtima ndi kundiyankha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu Yehova mundichitire chifundo ndipo mundiyankhe. |
Penyani, ndiyankheni, Yehova Mulungu wanga. Penyetsani maso anga, kuti ndingagone tulo ta imfa;
Munasanduliza kulira kwanga kukhale kusekera; munandivula chiguduli changa, ndipo munandiveka chikondwero,
Pakuti moyo wanga watha ndi chisoni, ndi zaka zanga zatha ndi kuusa moyo. Mphamvu yanga yafooka chifukwa cha kusakaza kwanga, ndi mafupa anga apuwala.
Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.
Tamvetsani mau a kufuula kwanga, Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga; pakuti kwa Inu ndimapemphera.