Masalimo 27:12 - Buku Lopatulika Musandipereke ku chifuniro cha akundisautsa, chifukwa zinandiukira mboni zonama ndi iwo akupumira zachiwawa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Musandipereke ku chifuniro cha akundisautsa, chifukwa zinandiukira mboni zonama ndi iwo akupumira zachiwawa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musandipereke m'manja mwa adani angawo. Mboni zonama zandiwukira, ndipo zimandiwopseza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musandipereke ku zokhumba za adani anga, pakuti mboni zambiri zauka kutsutsana nane ndipo zikundiopseza. |
Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo, ndipo adzadalitsika padziko lapansi, ndipo musampereke ku chifuniro cha adani ake.
Ndipo ndinawalanga kawirikawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukulu pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira kumizinda yakunja.
Koma Saulo, wosaleka kupumira pa ophunzira a Ambuye kuopsa ndi kupha, ananka kwa mkulu wa ansembe,
Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.