Zebuloni adzakhala m'mphepete mwa nyanja; ndipo iye adzakhala dooko la ngalawa; ndipo malire ake adakhala pa Sidoni.
Masalimo 25:3 - Buku Lopatulika Inde, onse akuyembekezera Inu sadzachita manyazi; adzachita manyazi iwo amene achita monyenga kopanda chifukwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inde, onse akuyembekezera Inu sadzachita manyazi; adzachita manyazi iwo amene achita monyenga kopanda chifukwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zoonadi, onse okhulupirira Inu asaŵachititse manyazi, koma muchititse manyazi onse ochita dala zosakhulupirika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aliyense amene amayembekezera kwa Ambuye sadzachititsidwa manyazi koma achinyengo ndiwo adzachititsidwe manyazi ndipo sadzakhala ndi chodzitetezera. |
Zebuloni adzakhala m'mphepete mwa nyanja; ndipo iye adzakhala dooko la ngalawa; ndipo malire ake adakhala pa Sidoni.
Momwemo Saulo anafa, chifukwa cha kulakwa kwake analakwira Yehova, kulakwira mau a Yehova amene sanawasunge; ndiponso chifukwa cha kufunsira wobwebweta, kufunsirako,
Odzikuza achite manyazi, popeza anandichitira monyenga ndi bodza: Koma ine ndidzalingalira malangizo anu.
Taonani, monga maso a anyamata ayang'anira dzanja la ambuye wao, monga maso a adzakazi ayang'anira dzanja la mbuye wao wamkazi: Momwemo maso athu ayang'anira Yehova Mulungu wathu, kufikira atichitira chifundo.
Koma ine ndine nyongolotsi, si munthu ai, chotonza cha anthu, ndi wonyozedwa ndi anthu.
Yehova, musandichititse manyazi; pakuti ndafuulira kwa Inu, oipa achite manyazi, atonthole m'manda.
Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza, imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima, ndi kudzikuza ndi kunyoza.
Achite manyazi, nadodome iwo akukondwera chifukwa cha choipa chidandigwera. Avekeke ndi manyazi ndi kupunzika iwo akudzikuza pa ine.
Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko. Pakudulidwa oipa udzapenya.
Adzachita manyazi, nadzanthunthumira kwakukulu adani anga onse; adzabwerera, nadzachita manyazi modzidzimuka.
Ondida kopanda chifukwa achuluka koposa tsitsi la pamutu panga; ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu. Pamenepo andibwezetsa chosafunkha ine.
Iwo akuyembekeza Inu, Ambuye, Yehova wa makamu, asachite manyazi chifukwa cha ine, iwo ofuna Inu, Mulungu wa Israele, asapepulidwe chifukwa cha ine.
Adani a moyo wanga achite manyazi, nathawe; chotonza ndi chimpepulo zikute ondifunira choipa.
Ndipo adzanena tsiku limenelo, Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tamlindirira Iye, tidzakondwa ndi kusekerera m'chipulumutso chake.
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.
Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao aakulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.
Koma Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsa; chifukwa chake ondisautsa adzaphunthwa, sadzandilala; adzakhala ndi manyazi ambiri, chifukwa sanachite chanzeru, ngakhale ndi kunyazitsa kwamuyaya kumene sikudzaiwalika.
Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa; Mulungu wanga adzandimvera.
Koma chitero, kuti mau olembedwa m'chilamulo chao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda chifukwa.