Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.
Masalimo 24:8 - Buku Lopatulika Mfumu imene ya ulemerero ndani? Yehova wamphamvu ndi wolimba, Yehova wolimba kunkhondo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mfumu imene ya ulemerero ndani? Yehova wamphamvu ndi wolimba, Yehova wolimba kunkhondo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Ndi Chauta wanyonga ndi wamphamvu, Chauta ndiye ngwazi pa nkhondo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Yehova Wamphamvuzonse, Yehova ndiye wamphamvu pa nkhondo. |
Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.
Yehova achita ufumu; wadziveka ndi ukulu; wadziveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m'chuuno; dziko lomwe lokhalamo anthu likhakizika, silidzagwedezeka.
Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.
Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, kavalo woyera, ndipo womkwerayo anali nao uta; ndipo anampatsa korona; ndipo anatulukira wogonjetsa kuti akagonjetse.