Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga; ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwitsa zanu.
Masalimo 22:9 - Buku Lopatulika Pakuti Inu ndinu wondibadwitsa; wondikhulupiritsa pokhala ine pa bere la mai wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Inu ndinu wondibadwitsa; wondikhulupiritsa pokhala ine pa bere la mai wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe Inu ndinu amene mudalola kuti ndibadwe. Inu ndinu chikhulupiriro changa, mudandilera bwino ndili mwana woyamwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Komabe Inu ndinu amene munandibadwitsa, munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga. Munachititsa kuti ndizikudalirani ngakhale pa nthawi imene ndinkayamwa. |
Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga; ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwitsa zanu.
Inu munandigwiriziza kuyambira ndisanabadwe, kuyambira pa thupi la mai wanga wondichitira zokoma ndinu; ndidzakulemekezani kosalekeza.
Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.