Masalimo 22:30 - Buku Lopatulika Mbumba ya anthu idzamtumikira; kudzanenedwa za Ambuye ku mibadwo yakudza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mbumba ya anthu idzamtumikira; kudzanenedwa za Ambuye ku mibadwo yakudza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zidzukulu zam'tsogolo zidzatumikira Ambuye. Anthu adzauza mbadwo umene ukudzawo za Iye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zidzukulu zamʼtsogolo zidzamutumikira Iye; mibado ya mʼtsogolo idzawuzidwa za Ambuye. |
ndikadati, Ndidzafotokozera chotere, taonani, ndikadachita chosakhulupirika ndi mbadwo wa ana ako.
Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake.
ndipo musamayesa kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu kuti mwa miyala iyi Mulungu akhoza kuukitsira Abrahamu ana.
Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;