Aleluya. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.
Masalimo 22:25 - Buku Lopatulika Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukulu, zowinda zanga ndidzazichita pamaso pa iwo akumuopa Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukulu, zowinda zanga ndidzazichita pamaso pa iwo akumuopa Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira. Zimene ndidalonjeza ndidzazichita pamaso pa onse okumverani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira. Ndidzakwaniritsa lonjezo langa pamaso pa amene amaopa Inu. |
Aleluya. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.
Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu, ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga.