Kuti ndione chokomacho cha osankhika anu, kuti ndikondwere nacho chikondwerero cha anthu anu, kuti ndidzitamandire pamodzi ndi cholowa chanu.
Masalimo 22:23 - Buku Lopatulika Inu akuopa Yehova, mumlemekeze; inu nonse mbumba ya Yakobo, mumchitire ulemu; ndipo muchite mantha ndi Iye, inu nonse mbumba ya Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inu akuopa Yehova, mumlemekeze; inu nonse mbumba ya Yakobo, mumchitire ulemu; ndipo muchite mantha ndi Iye, inu nonse mbumba ya Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzati, “Inu omvera Chauta, mtamandeni Iye. Inu nonse ana a Yakobe mlemekezeni Iye, inu nonse ana a Israele, mchitireni Iye ulemu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu amene mumaopa Yehova mutamandeni! Inu zidzukulu zonse za Yakobo, mulemekezeni! Muopeni mwaulemu, inu zidzukulu zonse za Israeli! |
Kuti ndione chokomacho cha osankhika anu, kuti ndikondwere nacho chikondwerero cha anthu anu, kuti ndidzitamandire pamodzi ndi cholowa chanu.
Ndidzayamika Yehova kwakukulu pakamwa panga; ndi pakati pa anthu aunyinji ndidzamlemekeza.
Aleluya. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.
Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.
Ndidzakuyamikani, Ambuye, Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse.
Chifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani Inu, mzinda wa mitundu yakuopsa udzakuopani Inu.
Ndipo abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zinthu zonse anazimva, naziona, monga kunalankhulidwa kwa iwo.
Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.
Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.