Ambuye, mudzapenyererabe nthawi yanji? Bwezani moyo wanga kwa zakundiononga zao, wanga wa wokha kwa misona ya mkango.
Masalimo 22:21 - Buku Lopatulika ndipulumutseni m'kamwa mwa mkango; inde mwandiyankha ine ndili pa nyanga za njati. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipulumutseni m'kamwa mwa mkango; inde mwandiyankha ine ndili pa nyanga za njati. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pulumutseni kukamwa kwa mkango, mulanditse moyo wanga wovutika ku nyanga za njati. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndilanditseni mʼkamwa mwa mikango; pulumutseni ku nyanga za njati. |
Ambuye, mudzapenyererabe nthawi yanji? Bwezani moyo wanga kwa zakundiononga zao, wanga wa wokha kwa misona ya mkango.
Ndipo njati zidzatsika ndi iwo, ndi ng'ombe zofula ndi zamphongo; ndi dziko laolao lidzanona ndi mafuta.
Masiku onse, pamene ndinali ndi inu mu Kachisi, simunatanse manja anu kundigwira: koma nyengo ino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa mdima ndi wanu.
Sindidzalankhulanso zambiri ndi inu, pakuti mkulu wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa Ine;
Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m'mzinda muno Herode, ndi Pontio Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israele kumchitira choipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza;
Woyamba kubadwa wa ng'ombe yake, ulemerero ndi wake; nyanga zake ndizo nyanga zanjati; adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi, kufikira malekezero a dziko lapansi. Iwo ndiwo zikwi khumi za Efuremu, iwo ndiwo zikwi za Manase.
Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.
Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire: