Iwo anandiyasamira pakamwa pao; anandiomba pama ndi kunditonza; asonkhana pamodzi kunditsutsa.
Masalimo 22:13 - Buku Lopatulika Andiyasamira m'kamwa mwao, ngati mkango wozomola ndi wobangula. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Andiyasamira m'kamwa mwao, ngati mkango wozomola ndi wobangula. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Andiyasamira kukamwa, ngati mkango wobangula wofuna kundikadzula. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mikango yobangula pokadzula nyama, yatsekula kwambiri pakamwa pawo kulimbana nane. |
Iwo anandiyasamira pakamwa pao; anandiomba pama ndi kunditonza; asonkhana pamodzi kunditsutsa.
Ambuye, mudzapenyererabe nthawi yanji? Bwezani moyo wanga kwa zakundiononga zao, wanga wa wokha kwa misona ya mkango.
Adani ako onse ayasamira pa iwe, atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza; ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona.
Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire: