Pakuti Yehova anapenya kuti kuzunzika kwao kwa Israele nkowawa ndithu; popeza panalibe womangika kapena womasuka, ndipo panalibe womthandiza Israele.
Masalimo 22:11 - Buku Lopatulika Musandikhalire kutali; pakuti nsautso ili pafupi, pakuti palibe mthandizi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Musandikhalire kutali; pakuti nsautso ili pafupi, pakuti palibe mthandizi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musandikhalire kutali, pakuti mavuto ali pafupi kundigwera, ndipo palibe wina wondithandiza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musakhale kutali ndi ine, pakuti mavuto ali pafupi ndipo palibe wina wondipulumutsa. |
Pakuti Yehova anapenya kuti kuzunzika kwao kwa Israele nkowawa ndithu; popeza panalibe womangika kapena womasuka, ndipo panalibe womthandiza Israele.
Inu munandigwiriziza kuyambira ndisanabadwe, kuyambira pa thupi la mai wanga wondichitira zokoma ndinu; ndidzakulemekezani kosalekeza.
Ndipo ndinayang'ana, koma panalibe wothangata; ndipo ndinadabwa kuti panalibe wochirikiza; chifukwa chake mkono wangawanga unanditengera chipulumutso, ndi ukali wanga unandichirikiza Ine.
Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa.
Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira, kuti, Sindidziwa munthuyo. Ndipo pompo tambala analira.
Onani ikudza nthawi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense ku zake za yekha, ndipo mudzandisiya Ine pa ndekha. Ndipo sindikhala pa ndekha, chifukwa Atate ali pamodzi ndi Ine,
Popeza Yehova adzaweruza anthu ake, nadzachitira nsoni anthu ake; pakuona Iye kuti mphamvu yao yatha, wosatsala womangika kapena waufulu.
Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,