Mverani Ine, zisumbu inu, mumvere anthu inu akutali; Yehova anandiitana Ine ndisanabadwe; m'mimba mwa amai Iye anatchula dzina langa;
Masalimo 22:10 - Buku Lopatulika Chibadwire ine anandisiyira Inu, kuyambira kwa mai wanga Mulungu wanga ndinu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chibadwire ine anandisiyira Inu, kuyambira kwa mai wanga Mulungu wanga ndinu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndakhala ndikudalira Inu chibadwire changa, Inu mwakhala Mulungu wanga kuyambira pamene mai wanga adandibala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chibadwire ine ndinaperekedwa kwa Inu; kuchokera mʼmimba mwa amayi anga Inu mwakhala muli Mulungu wanga. |
Mverani Ine, zisumbu inu, mumvere anthu inu akutali; Yehova anandiitana Ine ndisanabadwe; m'mimba mwa amai Iye anatchula dzina langa;
Ndisanakulenge iwe m'mimba ndinakudziwa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe; ndinakuika kuti ukhale mneneri wa mitundu ya anthu.
Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.
Ndipo Yesu anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.
Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu.
Koma pamene padakondweretsa Mulungu, amene anandipatula, ndisanabadwe, nandiitana ine mwa chisomo chake,