Koma ine ndakhulupirira pa chifundo chanu; mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu.
Masalimo 21:7 - Buku Lopatulika Pakuti mfumu akhulupirira Yehova, ndipo mwa chifundo cha Wam'mwambamwamba sadzagwedezeka iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti mfumu akhulupirira Yehova, ndipo mwa chifundo cha Wam'mwambamwamba sadzagwedezeka iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja mfumuyo imakhulupirira Chauta, ndipo siidzagwedezeka chifukwa cha chikondi chosasinthika cha Wopambanazonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti mfumu imadalira Yehova; kudzera mʼchikondi chake chosatha cha Wammwambamwamba, iyo sidzagwedezeka. |
Koma ine ndakhulupirira pa chifundo chanu; mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu.
Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.
Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.
Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda mu ungwiro wanga, ndipo ndakhulupirira Yehova, sindadzaterereka.
Dzimangireni lupanga lanu m'chuuno mwanu, wamphamvu inu, ndi ulemerero wanu ndi ukulu wanu.
Dzina lake lidzakhala kosatha, momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu. Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye; amitundu onse adzamutcha wodala.
Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.
Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka.
Amakhulupirira Mulungu; Iye ampulumutse tsopano, ngati amfuna; pakuti anati, Ine ndine Mwana wa Mulungu.
Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi chisoni, yense chifukwa cha ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wake.