Ndipo ichinso chinali pamaso panu chinthu chaching'ono, Yehova Mulungu; koma munanenanso za banja la mnyamata wanu kufikira nthawi yaikulu ilinkudza; ndipo mwatero monga mwa machitidwe a anthu, Yehova Mulungu!
Masalimo 21:5 - Buku Lopatulika Ulemerero wake ngwaukulu mwa chipulumutso chanu; mumchitira iye ulemu ndi ukulu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ulemerero wake ngwaukulu mwa chipulumutso chanu; mumchitira iye ulemu ndi ukulu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ulemerero wake ndi waukulu chifukwa mwaipambanitsa ndinu. Mwaipatsa ufumu waukulu ndi waulemu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kudzera mʼzigonjetso zimene munapereka, ulemerero wake ndi waukulu; Inu mwapereka pa iyo ulemerero ndi ufumu. |
Ndipo ichinso chinali pamaso panu chinthu chaching'ono, Yehova Mulungu; koma munanenanso za banja la mnyamata wanu kufikira nthawi yaikulu ilinkudza; ndipo mwatero monga mwa machitidwe a anthu, Yehova Mulungu!
Ndipo ukadzayenda m'njira zanga kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga atate wako Davide anayendamo, Ine ndidzachulukitsa masiku ako.
chakukomerani kudalitsa nyumba ya mtumiki wanu, kuti ikhalebe kosatha pamaso panu; pakuti Inu Yehova mwadalitsa, ndipo idzadalitsika kosatha.
Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.
Ngati mame a ku Heremoni, akutsikira pa mapiri a Ziyoni. Pakuti pamenepo Yehova analamulira dalitsolo, ndilo moyo womka muyaya.
Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.
Pa Mulungu pali chipulumutso changa ndi ulemerero wanga. Thanthwe la mphamvu yanga ndi pothawirapo panga mpa Mulungu.
Pamaso pake pali ulemu ndi ukulu. M'malo opatulika mwake muli mphamvu ndi zochititsa kaso.
Ndani uyu alikudza kuchokera ku Edomu, ndi zovala zonyika zochokera ku Bozira? Uyu wolemekezeka m'chovala chake, nayenda mu ukulu wa mphamvu zake? Ndine amene ndilankhula m'cholungama, wa mphamvu yakupulumutsa.
Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.
Zinthu izi analankhula Yesu; ndipo m'mene anakweza maso ake Kumwamba, anati, Atate, yafika nthawi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeni Inu;
Ndipo ulemerero umene mwandipatsa Ine ndapatsa iwo; kuti akhale amodzi, monga Ife tili mmodzi;
Ndipo tsopano, Atate Inu, lemekezani Ine ndi Inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nao ndi Inu lisanakhale dziko lapansi.
Koma mutu wa izi tanenazi ndi uwu: Tili naye Mkulu wa ansembe wotere, amene anakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Ukulu mu Kumwamba,
amene akhala padzanja lamanja la Mulungu, atalowa mu Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera.