Masalimo 21:2 - Buku Lopatulika Mwampatsa iye chikhumbo cha mtima wake, ndipo simunakane pempho la milomo yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mwampatsa iye chikhumbo cha mtima wake, ndipo simunakana pempho la milomo yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwaipatsa zimene mtima wake umakhumba, simudaimane zimene pakamwa pake padapempha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mwayipatsa zokhumba za mtima wake ndipo simunayimane zopempha za pa milomo yake. Sela |
Diso langa lapenya chokhumba ine pa iwo ondilalira, m'makutu mwanga ndamva chokhumba ine pa iwo akuchita zoipa akundiukira.
kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.
Ndipo Hana anapemphera, nati, Mtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova, nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova; pakamwa panga pakula kwa adani anga; popeza ndikondwera m'chipulumutso chanu.