Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi chipambano, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi padziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.
Masalimo 21:13 - Buku Lopatulika Kwezekani, Yehova, mu mphamvu yanu; potero tidzaimba ndi kulemekeza chilimbiko chanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kwezekani, Yehova, mu mphamvu yanu; potero tidzaimba ndi kulemekeza chilimbiko chanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mutamandike, Inu Chauta, chifukwa cha kupambana kwanu. Tidzaimba ndi kuyamika mphamvu zanu zazikulu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mukwezeke Inu Yehova mʼmphamvu yanu, ife tidzayimba nyimbo ndi kutamanda mphamvu yanu. |
Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi chipambano, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi padziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.
Yehova ngwa moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa; nakwezeke Mulungu wa chipulumutso changa.
Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi.
Kwezekani m'mwambamwamba, Mulungu; ulemerero wanu ukhale pamwamba m'dziko lonse lapansi.
Mukwezeke m'mwambamwamba, Mulungu; ulemerero wanu ukhale pamwamba padziko lonse lapansi.
nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli, nimunali; popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikulu, ndipo mwachita ufumu.
Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.