Masalimo 21:11 - Buku Lopatulika Pakuti anakupangirani choipa, anapangana chiwembu, osakhoza kuchichita. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti anakupangirani choipa, anapangana chiwembu, osakhoza kuchichita. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akafuna kuti aichite choipa ndi kuipweteka, adzalephereratu, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngakhale iwo akukonzereni chiwembu mwa kuchenjera kwawo sadzapambana; |
Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri, mantha andizinga. Pondipangira chiwembu, anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.
Amati, Tiyeni tiwaononge asakhalenso mtundu wa anthu; ndipo dzina la Israele lisakumbukikenso.
Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, awa ndi anthu olingirira za mphulupulu, ndi kupangira uphungu woipa m'mzinda muno;
Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta mu Betelehemu ndi ta m'midzi yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo.
Nawatumiza ku Betelehemu, nati, Yendani mufunitsitse za kamwanako; ndipo pamene mudzampeza, mundibwezere mau, kuti inenso ndidzadze kudzamlambira Iye.