koma wakukhudza iyo adzikonzeratu chitsulo ndi luti la mkondo; ndipo idzatenthedwa konse ndi moto m'malo mwao.
Masalimo 21:10 - Buku Lopatulika Mudzaziononga zobala zao kuzichotsa padziko lapansi, ndi mbeu zao mwa ana a anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mudzaziononga zobala zao kuzichotsa pa dziko lapansi, ndi mbeu zao mwa ana a anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mfumuyo idzaononga ana ao pa dziko lapansi, zidzukulu zao zidzatha pakati pa anthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mudzawononga ana awo pa dziko lapansi, zidzukulu zawo pakati pa anthu. |
koma wakukhudza iyo adzikonzeratu chitsulo ndi luti la mkondo; ndipo idzatenthedwa konse ndi moto m'malo mwao.
Ndimo umu munali tchimo la nyumba ya Yerobowamu, limene linaidula ndi kuiononga padziko lapansi.
Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.
Iwe sudzaphatikizidwa pamodzi nao poikidwa, pakuti iwe waononga dziko lako, wapha anthu ako; mbeu ya ochita zoipa sidzatchulidwa konse.
Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.