Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu; tcherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga.
Masalimo 20:9 - Buku Lopatulika Yehova, pulumutsani, mfumuyo ativomereze tsiku lakuitana ife. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova, pulumutsani, mfumuyo ativomereze tsiku lakuitana ife. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Chauta, thandizani mfumu kuti ipambane. Mutiyankhe pamene tikuitana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu Yehova, pulumutsani mfumu! Tiyankheni pamene tikuyitanani! |
Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu; tcherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga.
Weramutsani mitu yanu, zipata inu; ndipo kwezekani inu, zitseko zosatha, kuti Mfumu ya ulemerero ilowe.
Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga! Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya; mwawathyola mano oipawo.
Tamvetsani mau a kufuula kwanga, Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga; pakuti kwa Inu ndimapemphera.
Koma Mulungu ndiye mfumu yanga kuyambira kale, wochita zakupulumutsa pakati padziko lapansi.
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.
Koma ansembe aakulu ndi alembi, m'mene anaona zozizwitsa zomwe Iye anazichita, ndi ana alinkufuula ku Kachisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima,
Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!