Watonza Yehova mwa mithenga yako, nuti, Ndi magaleta anga aunyinji ndakwera pa misanje ya mapiri ku mbali zake za Lebanoni, ndipo ndidzagwetsa mikungudza yake yaitali, ndi mitengo yake yosankhika yamlombwa, ndidzalowanso m'ngaka mwake mwenimweni, ku nkhalango zake za madimba.
Pakuti ndinachita manyazi kupempha kwa mfumu gulu la asilikali, ndi apakavalo, kutithandiza pa adani panjira; popeza tidalankhula ndi mfumu kuti, Dzanja la Mulungu wathu likhalira mokoma onse akumfuna; koma mphamvu yake ndi mkwiyo wake zitsutsana nao onse akumsiya.
Ndipo anatuluka, iwo ndi makamu ao onse nao, anthu ambiri, kuchuluka kwao ngati mchenga uli m'mphepete mwa nyanja; ndi akavalo ndi magaleta ambirimbiri.
Ndipo Davide anati kwa Mfilistiyo, Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m'dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israele amene iwe unawanyoza.