M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso:
Masalimo 20:5 - Buku Lopatulika Tidzafuula mokondwera mwa chipulumutso chanu, ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera; Yehova akwaniritse mapempho ako onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tidzafuula mokondwera mwa chipulumutso chanu, ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera; Yehova akwaniritse mapempho ako onse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho tifuule ndi chimwemwe chifukwa chakuti mwapambana pa nkhondo, tikweze mbendera kutamanda dzina la Mulungu wathu. Chauta akupatse zonse zimene wapempha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu, Yehova ayankhe zopempha zako zonse. |
M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso:
Koma ine ndakhulupirira pa chifundo chanu; mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu.
Muyeso wao wapitirira padziko lonse lapansi, ndipo mau ao ku malekezero a m'dziko muli anthu. Iye anaika hema la dzuwa m'menemo,
Pakuti mufika kwa iye ndi madalitso okoma; muika korona wa golide woyengetsa pamutu pake.
Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse; pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni, ndidzakondwera nacho chipulumutso chanu.
Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Yese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pake padzakhala ulemerero.
Ndipo adzanena tsiku limenelo, Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tamlindirira Iye, tidzakondwa ndi kusekerera m'chipulumutso chake.
Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.
Pakuti mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m'dzina la mulungu wake, ndipo ife tidzayenda m'dzina la Yehova Mulungu wathu kunthawi yonka muyaya.
Pamenepo Eli anayankha nati, Pita ndi mtendere; ndipo Mulungu wa Israele akupatse chopempha chako unachipempha kwa Iye.
Ndipo Davide anati kwa Mfilistiyo, Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m'dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israele amene iwe unawanyoza.