Masalimo 20:2 - Buku Lopatulika likutumizire thandizo lotuluka m'malo oyera, ndipo likugwirizize kuchokera mu Ziyoni; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 likutumizire thandizo lotuluka m'malo oyera, ndipo likugwirizize kuchokera m'Ziyoni; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akutumizire chithandizo kuchokera ku malo ake oyera, akuchirikize kuchokera ku Ziyoni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye atumize thandizo kuchokera ku malo ake opatulika; akugwirizize kuchokera ku Ziyoni. |
Ndipo pamene adalowa nalo likasa la Mulungu analiika pamalo pake pakati pa hema amene Davide adaliutsira; ndipo Davide anapereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.
Ndipo anadulitsa ndi matabwa amkungudza mikono makumi awiri m'kati mwa nyumba m'tsogolo mwake, kuyambira pansi kulekeza kumitanda; ichi anamanga kukhala chipinda chamkati, malo opatulika kwambiri.
Pakuti alendo andiukira, ndipo oopsa afunafuna moyo wanga; sadziikira Mulungu pamaso pao.
Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.
Ndipo adzayankhanji amithenga a amitundu? Kuti Yehova wakhazikitsa Ziyoni, ndipo m'menemo anthu ake ovutidwa adzaona pobisalira.