Masalimo 19:6 - Buku Lopatulika Kutuluka kwake lituluka kolekezera thambo, ndipo kuzungulira kwake lifikira ku malekezero ake; ndipo kulibe kanthu kobisalira kutentha kwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kutuluka kwake lituluka kolekezera thambo, ndipo kuzungulira kwake lifikira ku malekezero ake; ndipo kulibe kanthu kobisalira kutentha kwake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Limatuluka kuyambira ku mathero ena a thambo, ndi kuzungulira mpaka ku mathero enanso. Palibe chinthu chilichonse chotha kulewa kutentha kwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambo ndi kuzungulira mpaka mbali inanso; palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake. |
ngatitu, mukhalabe m'chikhulupiriro, ochilimika ndi okhazikika ndi osasunthika kulekana nacho chiyembekezo cha Uthenga Wabwino umene mudaumva, wolalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo; umene ine Paulo ndakhala mtumiki wake.
Adani anu onse, Yehova, atayike momwemo. Koma iwo akukonda Inu akhale ngati dzuwa lotuluka mu mphamvu yake. Ndipo dziko linapumula zaka makumi anai.