Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 19:5 - Buku Lopatulika

ndipo lili ngati mkwati wakutuluka m'chipinda mwake, likondwera ngati chiphona kuthamanga m'njira.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndipo lili ngati mkwati wakutuluka m'chipinda mwake, likondwera ngati chiphona kuthamanga m'njira.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Dzuŵalo limatuluka ngati mkwati wokondwa amene akutuluka m'nyumba mwake, ndipo limayenda ndi chimwemwe ngati ngwazi yamphamvu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Dzuwa lili ngati mkwatibwi wobwera kuchokera ku nsanja yake, ngati katswiri wokondwerera kuthamanga pa mpikisano.

Onani mutuwo



Masalimo 19:5
8 Mawu Ofanana  

kuti agwire malekezero a dziko lapansi, nakutumule oipa achokeko?


Inde dzuwa lituluka, nililowa, nilifulumira komwe linatulukako.


Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.


Pakuti monga mnyamata akwatira namwali, momwemo ana ako aamuna adzakukwatira iwe; ndi monga mkwati akondwera ndi mkwatibwi, momwemo Mulungu wako adzakondwera nawe.


Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzake wa mkwatiyo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mau a mkwatiyo; chifukwa chake chimwemwe changa chimene chakwanira.