Masalimo 19:14 - Buku Lopatulika Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga zikhale zokondweretsa pamaso panu, Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga. |
Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga, ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu.
Atero Yehova, Mombolo wanu, Woyera wa Israele: Chifukwa cha inu ndatumiza ku Babiloni, ndipo ndidzatsitsira iwo onse monga othawa, ngakhale Ababiloni m'ngalawa za kukondwa kwao.
Atero Yehova, mfumu ya Israele ndi Mombolo wake, Yehova wa makamu, Ine ndili woyamba ndi womaliza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu.
Pakuti Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wa makamu ndiye dzina lake; ndi Woyera wa Israele ndiye Mombolo wako; Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.
kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.
ndi kulindirira Mwana wake achokere Kumwamba, amene anamuukitsa kwa akufa, Yesu, wotipulumutsa ife kumkwiyo ulinkudza.
amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.
Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, imene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mitulo yake; ndipo momwemo iye, angakhale adafa alankhulabe.
Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.
inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.
Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,