Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, Inde ndidziwa Ine, kuti wachita icho ndi mtima wangwiro, ndipo Inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine: chifukwa chake sindinakuloleze iwe kuti umkhudze mkaziyo.
Masalimo 19:13 - Buku Lopatulika Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine. Pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine. Pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musalole kuti ine mtumiki wanu ndizichimwa dala, kulakwa koteroku ndisakutsate. Tsono ndidzakhala wangwiro wopanda mlandu wa uchimo waukulu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muteteze mtumiki wanunso ku machimo ochita akudziwa; iwo asandilamulire. Kotero ndidzakhala wosalakwa, wopanda mlandu wa tchimo lalikulu. |
Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, Inde ndidziwa Ine, kuti wachita icho ndi mtima wangwiro, ndipo Inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine: chifukwa chake sindinakuloleze iwe kuti umkhudze mkaziyo.
Chimene sindichiona mundilangize ndi Inu, ngati ndachita chosalungama sindidzabwerezanso.
Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.
Koma munthu akachita dala pa mnzake, kumupha monyenga; uzimchotsa ku guwa langa la nsembe, kuti afe.
Ndipo gulu lonse la Israele likalakwa osati dala, ndipo chikabisika chinthuchi pamaso pa msonkhano, litachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, ndi kupalamula;
Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu;
Akachimwa mkulu, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova Mulungu wake, napalamula;
Ndipo akachimwa wina wa anthu a m'dziko, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, napalamula;
M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbumtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.
koma makamaka iwo akutsata za thupi, m'chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro; osaopa kanthu, otsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu aulemerero;
Ndipo pamene Davide anamva kuti Nabala adamwalira, iye anati, Alemekezedwe Yehova, amene anaweruza mlandu wa mtonzo wanga wochokera ku dzanja la Nabala, naletsa mnyamata wake pa choipa; ndipo Yehova anabwezera pamutu pa Nabala choipa chake. Ndipo Davide anatumiza wokamfunsira Abigaile, zakuti amtengere akhale mkazi wake.