Ndipo ukakudzerani mlandu uliwonse wochokera kwa abale anu okhala m'mizinda mwao, kusiyanitsa pakati pa mwazi ndi mwazi, pakati pa chilamulo ndi chiuzo, malemba ndi maweruzo, muwachenjeze kuti asapalamule kwa Yehova, angafikitsire inu nokha ndi abale anu mkwiyo; muzitero, ndipo simudzapalamula.
Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, dyetsa m'mimba mwako, nudzaze matumbo ako ndi mpukutu uwu ndakupatsawu. M'mwemo ndinaudya, ndi m'kamwa mwanga munazuna ngati uchi.
Ndipo iye pakuona ambiri a Afarisi ndi a Asaduki akudza ku ubatizo wake, anati kwa iwo, Obadwa a njoka inu, ndani anakulangizani kuthawa mkwiyo ulinkudza?
Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti ntchito zao zitsatana nao pamodzi.