Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yake; ndasungitsa mau a pakamwa pake koposa lamulo langalanga.
Masalimo 19:10 - Buku Lopatulika Ndizo zifunika koposa golide, inde, golide wambiri woyengetsa; zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndizo zifunika koposa golide, inde, golide wambiri woyengetsa; zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zonsezi nzoyenera kuzikhumbira kupambana golide, ngakhale golide wambiri wamtengowapatali, nzotsekemera kupambana uchi, ngakhale uchi wozuna kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndi a mtengowapatali kuposa golide, kuposa golide weniweni; ndi otsekemera kuposa uchi, kuposa uchi wochokera pa chisa chake. |
Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yake; ndasungitsa mau a pakamwa pake koposa lamulo langalanga.
Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona; ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakufuula mokondwera.
Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golide, kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?
Chipatso changa chiposa golide, ngakhale golide woyengeka; phindu langa liposa siliva wosankhika.
Ndipo ndinatenga kabuku m'dzanja la mngelo, ndipo ndinakadya; ndipo kanali m'kamwa mwanga kozuna ngati uchi; ndipo pamene ndinakadya m'mimba mwanga mudawawa.