M'kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova, inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga; ndipo Iye anamva mau anga ali mu Kachisi wake, ndi kulira kwanga kunafika ku makutu ake.
Masalimo 18:6 - Buku Lopatulika M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova, ndipo ndinakuwira Mulungu wanga; mau anga anawamva mu Kachisi mwake, ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m'makutu mwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova, ndipo ndinakuwira Mulungu wanga; mau anga anawamva m'Kachisi mwake, ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m'makutu mwake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidaitana Chauta m'zovuta zanga. Ndidafuulira Mulungu wanga kuti andithandize. Iye ali m'Nyumba mwake, adamva liwu langa, kulira kwanga kofuna chithandizo kudamveka kwa iye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova; ndinalirira kwa Mulungu wanga kuti andithandize. Ali mʼNyumba yake, anamva mawu anga; kulira kwanga kunafika pamaso pake ndi mʼmakutu mwake. |
M'kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova, inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga; ndipo Iye anamva mau anga ali mu Kachisi wake, ndi kulira kwanga kunafika ku makutu ake.
Pamenepo ansembe Alevi anauka, nadalitsa anthu; ndi mau ao anamveka, ndi pemphero lao lidakwera pokhala pake popatulika Kumwamba.
Yehova ali mu Kachisi wake woyera, Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.
Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu ndidzalowa m'nyumba yanu; ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.
Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aejipito; ndi ana a Israele anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo.
Koma Yehova ali mu Kachisi wake wopatulika; dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.
Ndipo ananena, Abba, Atate, zinthu zonse zitheka ndi Inu; mundichotsere chikho ichi; komatu si chimene ndifuna Ine, koma chimene mufuna Inu.
Pamenepo ndipo Petro anasungika m'ndende; koma Mpingo anampempherera iye kwa Mulungu kosalekeza.
Ndipo anatsegulidwa Kachisi wa Mulungu amene ali mu Mwamba; ndipo linaoneka likasa la chipangano chake, mu Kachisi mwake, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi chivomezi, ndi matalala aakulu.