Zingwe za imfa zinandizinga, ndi zowawa za manda zinandigwira: ndinapeza nsautso ndi chisoni.
Masalimo 18:5 - Buku Lopatulika Zingwe za manda zindizinga, misampha ya imfa inandifikira ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zingwe za manda zindizinga, misampha ya imfa inandifikira ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthambo zakumanda zidandizeŵeza, misampha ya imfa idandikola. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anandimanga ndi zingwe za ku manda; misampha ya imfa inalimbana nane. |
Zingwe za imfa zinandizinga, ndi zowawa za manda zinandigwira: ndinapeza nsautso ndi chisoni.
Mundiyankhe Yehova; pakuti chifundo chanu nchokoma; munditembenukire monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu.
Pakuti chifundo chanu cha pa ine nchachikulu; ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.
Pakuti munthu sadziwatu mphindi yake; monga nsomba zigwidwa mu ukonde woipa, ndi mbalame zikodwa mumsampha, momwemo ana a anthu amagwidwa ndi nthawi ya tsoka, ngati msampha umene uwagwera modzidzimuka.
yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe nayo.