Masalimo 18:47 - Buku Lopatulika Ndiye Mulungu amene andibwezerera chilango, nandigonjetsera mitundu ya anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiye Mulungu amene andibwezerera chilango, nandigonjetsera mitundu ya anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu ndiye adandithandiza kuti ndilipsire, adagonjetsa anthu a mitundu ina, kuti akhale mu ulamuliro wanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango, amene amagonjetsa anthu a mitundu yonse amene ali pansi pa ulamuliro wanga, |
Ndiye chifundo changa, ndi linga langa, msanje wanga, ndi Mpulumutsi wanga; chikopa changa, ndi Iye amene ndimtama; amene andigonjetsera anthu anga.
Yehova ndiye Mulungu wansanje, nabwezera chilango; Yehova ndiye wobwezera chilango, ndi waukali ndithu; Yehova ndiye wobwezera chilango oyambana naye, nasungira mkwiyo pa adani ake.
Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.
Kubwezera chilango nkwanga, kubwezera komwe, pa nyengo ya kuterereka phazi lao; pakuti tsiku la tsoka lao layandika, ndi zinthu zowakonzeratu zifulumira kudza.