Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuzayo, Kwanu nkuti? Nayankha, Ine ndine mwana wa mlendo, Mwamaleke.
Masalimo 18:44 - Buku Lopatulika Pakumva m'khutu za ine adzandimvera, alendo adzandigonjera monyenga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakumva m'khutu za ine adzandimvera, alendo adzandigonjera monyenga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atangomva za ine adayamba kundimvera, anthu a maiko ena adabwera kwa ine kudzapemba. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Alendo amadzipereka okha pamaso panga; akangomva za ine amandigonjera. |
Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuzayo, Kwanu nkuti? Nayankha, Ine ndine mwana wa mlendo, Mwamaleke.
Nenani kwa Mulungu, Ha, ntchito zanu nzoopsa nanga! Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu.
Dzudzulani chilombo cha m'bango, khamu la mphongo ndi ng'ombe za anthu, yense wakudzigonjera ndi ndalama za siliva; anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo.
Yehova analumbira padzanja lake lamanja, ndi mkono wake wamphamvu, Zoonadi, sindidzaperekanso tirigu wako akhale chakudya cha adani ako, ndipo alendo sadzamwa vinyo wako amene iwe unagwirira ntchito;
popeza mwalowa nao achilendo osadulidwa m'mtima, osadulidwa m'thupi akhale m'malo anga opatulika kuwadetsa, ndiwo nyumba yanga, popereka inu mkate wanga, mafuta, ndi mwazi; ndipo munathyola pangano langa pamodzi ndi zonyansa zanu zonse.
Wodala iwe, Israele; akunga iwe ndani, mtundu wa anthu opulumutsidwa ndi Yehova, ndiye chikopa cha thandizo lako, Iye amene akhala lupanga la ukulu wako! Ndi adani ako adzakugonjera; ndipo udzaponda pa misanje yao.