Ndidziwanso, Mulungu wanga, kuti muyesa mtima, nimukondwera nako kuongoka. Koma ine, ndi mtima wanga woongoka ndapereka zonsezi mwaufulu; ndipo tsopano ndaona mokondwera anthu anu okhala pompano, napereka kwa Inu mwaufulu.
Masalimo 18:23 - Buku Lopatulika Ndipo ndinakhala wangwiro ndi Iye, ndipo ndinadzisunga wosachita choipa changa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndinakhala wangwiro ndi Iye, ndipo ndinadzisunga wosachita choipa changa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndinalibe mlandu pamaso pake, ndinkalewa zoipa m'moyo mwanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo. |
Ndidziwanso, Mulungu wanga, kuti muyesa mtima, nimukondwera nako kuongoka. Koma ine, ndi mtima wanga woongoka ndapereka zonsezi mwaufulu; ndipo tsopano ndaona mokondwera anthu anu okhala pompano, napereka kwa Inu mwaufulu.
Mwayesera mtima wanga; mwandizonda usiku; mwandisuntha, simupeza kanthu; mwatsimikiza mtima kuti m'kamwa mwanga simudzalakwa.
Ndipo Yehova adzabwezera munthu yense chilungamo chake ndi chikhulupiriko chake, popeza Yehova anakuperekani lero m'dzanja langa, koma sindinalole kutukulira dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova.