Masalimo 18:22 - Buku Lopatulika Pakuti maweruzo ake onse anali pamaso panga, ndipo malemba ake sindinawachotse kwa ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti maweruzo ake onse anali pamaso panga, ndipo malemba ake sindinawachotsa kwa ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidamvera malangizo ake onse, ndipo malamulo ake sindidaŵataye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Malamulo ake onse ali pamaso panga; sindinasiye malangizo ake. |
Chifukwa chake ndiyesa ngolunjika malangizo anu onse akunena zonse; koma ndidana nazo njira zonse zonyenga.
Zitapita izi Yesu anampeza mu Kachisi, nati kwa iye, Taona, wachiritsidwa; usachimwenso, kuti chingakugwere choipa choposa.
Ndipo munene pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Ndachotsa zopatulika m'nyumba mwanga, ndi kuzipereka kwa Mlevi, ndi kwa mlendo, ndi kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, monga mwa lamulo lanu lonse munandilamulira ine; sindinalakwire malamulo anu, kapena kuwaiwala.
Sindinadyeko m'chisoni changa, kapena kuchotsako podetsedwa, kapena kuperekako kwa akufa; ndamvera mau a Yehova Mulungu wanga; ndachita monga mwa zonse munandilamulira ine.