Ndipo anayenda m'njira ya Asa atate wake osapatukamo, nachita zoongoka pamaso pa Yehova.
Masalimo 18:21 - Buku Lopatulika Pakuti ndasunga njira za Yehova, ndipo sindinachitire choipa kusiyana ndi Mulungu wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ndasunga njira za Yehova, ndipo sindinachitira choipa kusiyana ndi Mulungu wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ine ndidatsata njira za Chauta, sindidachite zoipa ndi kumsiya Mulungu wanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova; ndilibe mlandu wochoka pamaso Mulungu wanga. |
Ndipo anayenda m'njira ya Asa atate wake osapatukamo, nachita zoongoka pamaso pa Yehova.
Yosiya nachotsa zonyansa zonse m'maiko onse okhala a ana a Israele, natumikiritsa onse opezeka mu Israele, inde kutumikira Yehova Mulungu wao. Masiku ake onse iwo sanapatuke kusamtsata Yehova Mulungu wa makolo ao.
Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda mu ungwiro wanga, ndipo ndakhulupirira Yehova, sindadzaterereka.
Ithe mphulupulu ya anthu oipa, ndikupemphani, koma wolungamayo mumkhazikitse. Pakuti woyesa mitima ndi impso ndiye Mulungu wolungama.
Pamenepo mfumu inakondwera kwambiri, niwauza atulutse Daniele m'dzenje. Momwemo anamtulutsa Daniele m'dzenje, ndi pathupi pake sipadaoneke bala, popeza anakhulupirira Mulungu wake.
M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbumtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.
Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira;
Anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero kuti aonekere kuti sali onse a ife.
Kundichititsa chisoni kuti ndinaika Saulo akhale mfumu; pakuti wabwerera wosanditsata Ine, ndipo sanachite malamulo anga. Ndipo Samuele anakwiya; nalira kwa Yehova usiku wonse.