Amene alumikiza mitanda ya zipinda zake m'madzi; naika makongwa akhale agaleta ake; nayenda pa mapiko a mphepo.
Masalimo 18:11 - Buku Lopatulika Anaika mdima pobisala pake, hema wake womzinga; mdima wa madzi, makongwa a kuthambo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anaika mdima pobisala pake, hema wake womzinga; mdima wa madzi, makongwa a kuthambo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mdima adausandutsa chofunda chake, mitambo yakuda yamvula adaisandutsa mwafuli wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anapanga mdima kukhala chofunda chake, chophimba chake chomuzungulira chinali mitambo yakuda ya mlengalenga. |
Amene alumikiza mitanda ya zipinda zake m'madzi; naika makongwa akhale agaleta ake; nayenda pa mapiko a mphepo.
Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake, adzandibisa mkati mwa chihema chake; pathanthwe adzandikweza.
Unaitana posautsika, ndipo ndinakulanditsa; ndinakuvomereza mobisalika m'bingu; ndinakuyesa kumadzi a Meriba.
Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.
Pomzinga pali mitambo ndi mdima; chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa mpando wake wachifumu.
tsiku la mdima, la mdima wandiweyani, tsiku la mitambo, mitambo yochindikira, ngati m'mbandakucha moyalika pamapiri; mtundu waukulu ndi wamphamvu, panalibe wotere ndi kale lonse, sipadzakhalanso wotere utapita uwu, kufikira zaka za mibadwo yambiri.
Ndipo munayandikiza ndi kuima patsinde paphiri; ndi phirilo linayaka moto kufikira pakati pa thambo; kunali mdima, ndi mtambo, inde mdima bii.