Amene alumikiza mitanda ya zipinda zake m'madzi; naika makongwa akhale agaleta ake; nayenda pa mapiko a mphepo.
Masalimo 18:10 - Buku Lopatulika Ndipo anaberekeka pa kerubi, nauluka; nauluka msanga pa mapiko a mphepo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anaberekeka pa kerubi, nauluka; nauluka msanga pa mapiko a mphepo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adakwera pa mkerubi nauluka. Adayenda mwaliŵiro ndi mphepo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anakwera pa Kerubi ndi kuwuluka; nawuluka ndi mphepo mwaliwiro. |
Amene alumikiza mitanda ya zipinda zake m'madzi; naika makongwa akhale agaleta ake; nayenda pa mapiko a mphepo.
Mbusa wa Israele, tcherani khutu; inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa; inu wokhala pa akerubi, walitsani.
Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere; Iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke.
Ife takhala ngati iwo amene simunawalamulire konse, ngati iwo amene sanatchedwe dzina lanu.