Masalimo 17:6 - Buku Lopatulika Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu; tcherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu; tcherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikupemphera kwa Inu Mulungu, chifukwa mudzandiyankha. Tcherani khutu kuti mumve mau anga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndikuyitana Inu, Mulungu wanga, pakuti mudzandiyankha; tcherani khutu lanu kwa ine ndipo mumve pemphero langa. |
Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe. Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete.
Tcherani makutu anu, Yehova, nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimuone; ndi kumva mau onse a Senakeribu, amene watumiza kumtonza Mulungu wamoyo.
Chifukwa chake, Yehova, Mulungu wathu, mutipulumutse ife m'manja mwake, kuti maufumu onse a dziko adziwe, kuti Inu ndinu Yehova, Inu nokha.