Alalira monga mkango m'ngaka mwake; alalira kugwira wozunzika, agwira wozunzika, pakumkola mu ukonde mwake.
Masalimo 17:12 - Buku Lopatulika Afanana ndi mkango wofuna kumwetula, ndi msona wa mkango wakukhala mobisalamo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Afanana ndi mkango wofuna kumwetula, ndi msona wa mkango wakukhala mobisalamo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ali ngati mkango wofunitsitsa kuti ukadzule, ngati chilombo cholusa cholalira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo ali ngati mkango wofuna nyama; ngati mkango waukulu wokhala mobisala. |
Alalira monga mkango m'ngaka mwake; alalira kugwira wozunzika, agwira wozunzika, pakumkola mu ukonde mwake.
Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.
Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire: