Popeza anakuta nkhope yake ndi kunenepa kwake, nachita mafunyenye a mafuta m'zuuno zake;
Masalimo 17:10 - Buku Lopatulika Mafuta ao awatsekereza; m'kamwa mwao alankhula modzikuza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mafuta ao awatsekereza; m'kamwa mwao alankhula modzikuza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mitima yao ilibe chifundo, amalankhula modzikuza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo amatseka mitima yawo yopanda chifundo, ndi pakamwa pawo amayankhula modzitamandira. |
Popeza anakuta nkhope yake ndi kunenepa kwake, nachita mafunyenye a mafuta m'zuuno zake;
Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza, imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima, ndi kudzikuza ndi kunyoza.
Mdani anati, Ndiwalondola, ndiwapeza, ndidzagawa zofunkha; ndidzakhuta nao mtima; ndidzasolola lupanga langa, dzanja langa lidzawaononga.
Koma Farao anati, Yehova ndani, kuti ndimvere mau ake ndi kulola Israele apite? Sindimdziwa Yehova, ndiponso sindidzalola Israele apite.
Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu ao, nutseke maso ao; angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angazindikire ndi mtima wao, nakabwerenso, nachiritsidwe.
Chifukwa unalemera mtima wa anthu awa, ndipo m'makutu ao anamva mogontha, ndipo maso ao anatsinzina; kuti asaone konse ndi maso, asamve ndi makutu, asazindikire ndi mtima wao, asatembenuke, ndipo ndisawachiritse iwo.
pakuti mtima wa anthu awa watupatu, ndipo m'makutu mwao mmolema kumva, ndipo maso ao anawatseka; kuti angaone ndi maso, nangamve ndi makutu, nangazindikire ndi mtima, nangatembenuke, ndipo Ine ndingawachiritse.
Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira; wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta; pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga, napeputsa thanthwe la chipulumutso chake.
Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, anthu amene adayamba kupulumuka kwa iwo a mayendedwe olakwa;
Musalankhulenso modzikuza kwambiri motero; m'kamwa mwanu musatuluke zolulutsa; chifukwa Yehova ndi Mulungu wanzeru, ndipo Iye ayesa zochita anthu.