Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala ya sulufure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao.
Masalimo 16:5 - Buku Lopatulika Yehova ndiye gawo la cholowa changa ndi chikho changa, ndinu wondigwirira cholandira changa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova ndiye gawo la cholowa changa ndi chikho changa, ndinu wondigwirira cholandira changa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta ndiye chuma changa ndi choloŵa changa. Tsogolo langa lili m'manja mwanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova, Inu mwandipatsa cholowa changa ndi chikho changa; mwateteza kolimba gawo langa. |
Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala ya sulufure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao.
Pakuti ndodo yachifumu ya choipa siidzapumula pa gawo la olungama; kuti olungama asatulutse dzanja lao kuchita chosalungama.
Yehova analumbira Davide zoona; sadzalibweza; ndi kuti, Wa iwo okhala zipatso za thupi lako ndidzaika pa mpando wachifumu wako.
Ndinafuulira kwa inu, Yehova; ndinati, Inu ndinu pothawirapo panga, gawo langa m'dziko la amoyo.
Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.
Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.
Ndidzakhazika mbeu yako kunthawi yonse, ndipo ndidzamanga mpando wachifumu wako ku mibadwomibadwo.
Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.
Chifukwa chake ndidzamgawira gawo ndi akulu; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wake kuimfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula machimo a ambiri, napembedzera olakwa.
Gawo la Yakobo silifanana ndi iwo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndiye mtundu wa cholowa chake; dzina lake ndi Yehova wa makamu.
Ameneyo Mulungu anamkweza ndi dzanja lake lamanja, akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israele kulapa, ndi chikhululukiro cha machimo.
Alibe cholowa pakati pa abale ao; Yehova mwini wake ndiye cholowa chao, monga ananena nao.
Pakuti Yehova anaika Yordani ukhale malire pakati pa ife ndi inu, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi; mulibe gawo ndi Yehova; motero ana anu adzaleketsa ana athu asaope Yehova.
koma lidzakhala mboni pakati pa ife ndi inu, ndi pakati pa mibadwo yathu ya m'tsogolo, kuti tikachita ntchito ya Yehova pamaso pake ndi nsembe zathu zopsereza, ndi zophera, ndi zoyamika; kuti ana anu asanene ndi ana athu m'tsogolomo, Mulibe gawo ndi Yehova.