Masalimo 16:11 - Buku Lopatulika Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mumandiwonetsa njira ya ku moyo. Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu, ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mwandidziwitsa njira ya moyo; mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu, ndidzasangalala mpaka muyaya pa dzanja lanu lamanja. |
Koma ine ndidzapenyerera nkhope yanu m'chilungamo, ndidzakhuta mtima ndi maonekedwe anu, pamene ndidzauka.
Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.
Imbirani Mulungu, liimbireni nyimbo dzina lake; undirani mseu Iye woberekekayo kuchidikha; dzina lake ndiye Yehova; ndipo tumphani ndi chimwemwe pamaso pake.
Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.
sasinkhasinkha bwino za njira ya moyo; mayendedwe ake adzandira dzandidzandi osadziwa iye.
Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ake; chifukwa mu Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mau a Yehova kuchokera mu Yerusalemu.
Ndipo amenewa adzachoka kunka ku chilango cha nthawi zonse; koma olungama kumoyo wa nthawi zonse.
Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka.
Pamenepo Ambuye Yesu, atatha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala padzanja lamanja la Mulungu.
nati, Taonani, ndipenya mu Mwamba motseguka, ndi Mwana wa Munthu alikuimirira padzanja lamanja la Mulungu.
Koma ngati Mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Khristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu.
Pakuti tsopano tipenya m'kalirole, ngati chimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa.
Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero;
ndi kuzama nchiyani; ndi kuzindikira chikondi cha Khristu, chakuposa mazindikiridwe, kuti mukadzazidwe kufikira chidzalo chonse cha Mulungu.
chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.
amene akhala padzanja lamanja la Mulungu, atalowa mu Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera.
Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali.
Ndipo kwa Iye amene akhoza kukudikirani mungakhumudwe, ndi kukuimikani pamaso pa ulemerero wake opanda chilema m'kukondwera,
Ndipo sikudzakhalanso usiku; ndipo sasowa kuunika kwa nyali, ndi kuunika kwa dzuwa; chifukwa Ambuye Mulungu adzawaunikira; ndipo adzachita ufumu kunthawi za nthawi.