Mwana wamkazi wa ku Babiloni, iwe amene udzapasulidwa; wodala iye amene adzakubwezera chilango monga umo unatichitira ife.
Masalimo 149:9 - Buku Lopatulika kuwachitira chiweruzo cholembedwacho. Ulemu wa okondedwa ake onse ndi uwu. Aleluya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuwachitira chiweruzo cholembedwacho. Ulemu wa okondedwa ake onse ndi uwu. Aleluya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa kuti aŵalange monga momwe Mulungu adalamulira. Umenewu ndiwo ulemerero wa anthu okhulupirira Chauta. Tamandani Chauta! Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kuchita zimene zinalembedwa zotsutsana nawo Uwu ndi ulemerero wa oyera mtima ake onse. Tamandani Yehova. |
Mwana wamkazi wa ku Babiloni, iwe amene udzapasulidwa; wodala iye amene adzakubwezera chilango monga umo unatichitira ife.
Ndipo anakweza nyanga ya anthu ake, chilemekezo cha okondedwa ake onse; ndiwo ana a Israele, anthu a pafupi pa Iye. Aleluya.
Nadzakhalamo osatekeseka, nadzamanga nyumba, ndi kuoka mpesa m'mindamo, nadzakhalamo mosatekeseka, ndikatha kukwaniritsira maweruzo pa onse akuwapeputsa pozungulira pao; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao.
ndikanola lupanga langa lonyezimira, ndi dzanja langa likagwira chiweruzo; ndidzabwezera chilango ondiukira, ndi kulanga ondida.
Iye wakupambana, ndidzampatsa akhale pansi ndi Ine pa mpando wachifumu wanga, monga Inenso ndinapambana, ndipo ndinakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wachifumu wake.