Masalimo 149:8 - Buku Lopatulika kumanga mafumu ao ndi maunyolo, ndi omveka ao ndi majerejede achitsulo, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kumanga mafumu ao ndi maunyolo, ndi omveka ao ndi majerejede achitsulo, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amange mafumu ao ndi maunyolo, amange atsogoleri ao ndi zitsulo, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kumanga mafumu awo ndi zingwe, anthu awo otchuka ndi unyolo wachitsulo, |
Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene Yoswa ndi ana a Israele anawakantha tsidya lija la Yordani kumadzulo, kuyambira Baala-Gadi m'chigwa cha Lebanoni mpaka phiri la Halaki lokwera kunka ku Seiri; ndipo Yoswa analipereka kwa mafuko a Israele, likhale laolao, monga mwa magawo ao;