Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzoona, ndi njira zake chiweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwachepetsa.
Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.
Ndipo m'dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndi m'kamwa mwake mudatuluka lupanga lakuthwa konsekonse; ndipo nkhope yake ngati dzuwa lowala mu mphamvu yake.
Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, ndi kunena, Aleluya; pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.