Chomwecho Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anakwera nalo likasa la Yehova, ndi chimwemwe ndi kulira kwa malipenga.
Masalimo 149:5 - Buku Lopatulika Okondedwa ake atumphe mokondwera mu ulemu: Afuule mokondwera pamakama pao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Okondedwa ake atumphe mokondwera m'ulemu: Afuule mokondwera pamakama pao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Okhulupirika akondwerere chigonjetso chopambanachi, aziimba mokondwa ali gone pa mabedi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Oyera mtima asangalale mu ulemu wake ndi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo. |
Chomwecho Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anakwera nalo likasa la Yehova, ndi chimwemwe ndi kulira kwa malipenga.
M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso:
Ndipo ansembe ake ndidzawaveka ndi chipulumutso: Ndi okondedwa ake adzafuulitsa mokondwera.
Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake, ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine. Inde pemphero la kwa Mulungu wa moyo wanga.
ndi mlandu unakomera opatulika a Wam'mwambamwamba, nifika nthawi yakuti ufumu unali wao wa opatulikawo.
amene ife tikhoza kulowa naye ndi chikhulupiriro m'chisomo ichi m'mene tilikuimamo; ndipo tikondwera m'chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu.
amene mungakhale simunamuone mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero: