Ndipo Davide anavina ndi mphamvu yake yonse pamaso pa Yehova; Davide nadzimangirira efodi wabafuta.
Masalimo 149:3 - Buku Lopatulika Alemekeze dzina lake ndi kuthira mang'ombe; amuimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Alemekeze dzina lake ndi kuthira mang'ombe; amuimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atamande dzina lake povina, amuimbire nyimbo yokoma ndi ng'oma ndi pangwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atamande dzina lake povina ndi kuyimbira Iye nyimbo ndi tambolini ndi pangwe. |
Ndipo Davide anavina ndi mphamvu yake yonse pamaso pa Yehova; Davide nadzimangirira efodi wabafuta.
Ndipo kunali pamene likasa la Yehova linafika m'mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikuvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwake.
ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi malipenga ndi nsanje za iwo akumveketsadi, ndi zoimbira nyimbo za Mulungu; ndi ana a Yedutuni anakhala kuchipata.
Onsewa anawalangiza ndi atate wao aimbe m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, zisakasa ndi azeze; atumikire nazo m'nyumba ya Mulungu; ndipo Asafu, Yedutuni, ndi Hemani, anawalangiza ndi mfumu.
Ndipo anafika ku Yerusalemu ndi zisakasa, ndi azeze, ndi malipenga, kunyumba ya Yehova.
Ndipo anaika Alevi m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, monga umo adauzira Davide, ndi Gadi mlauli wa mfumu, ndi Natani mneneriyo; pakuti lamulo ili lidafuma kwa Yehova mwa aneneri ake.
Ndipo pomanga maziko a Kachisi wa Yehova, amisiriwo anaimiritsa ansembe ovala zovala zao ndi mphalasa, ndi Alevi ana a Asafu ndi nsanje, kuti alemekeze Yehova, monga umo anaikiratu Davide mfumu ya Israele.
Munasanduliza kulira kwanga kukhale kusekera; munandivula chiguduli changa, ndipo munandiveka chikondwero,
Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.
Ndipo namwali adzasangalala m'masewero, ndi anyamata ndi nkhalamba pamodzi; pakuti ndidzasandutsa kulira kwao kukhale kukondwera, ndipo ndidzatonthoza mitima yao, ndi kuwasangalatsa iwo asiye chisoni chao.
Ndidzamangitsanso mudzi wako, ndipo udzamangidwa, iwe namwali wa Israele; udzakometsedwanso ndi mangaka, ndipo udzatulukira masewero a iwo akukondwerera.
Pofika Yefita ku Mizipa kunyumba yake, taonani, mwana wake wamkazi anatuluka kudzakomana naye ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe; ndipo iyeyu anali mwana wake mmodzi yekha, analibe mwana wina wamwamuna kapena wamkazi.