Aleluya. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.
Masalimo 149:1 - Buku Lopatulika Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tamandani Chauta! Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, imbani nyimbo yomtamanda pa msonkhano wa anthu ake oyera mtima. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tamandani Yehova. Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima. |
Aleluya. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.
Ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano, Mulungu; pa chisakasa cha zingwe khumi ndidzaimbira zakukulemekezani.
Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukulu, zowinda zanga ndidzazichita pamaso pa iwo akumuopa Iye.
Ndipo kumwamba kudzalemekeza zodabwitsa zanu, Yehova; chikhulupiriko chanunso mu msonkhano wa oyera mtima.
Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; popeza anachita zodabwitsa: Dzanja lake lamanja, mkono wake woyera, zinamchitira chipulumutso.
Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ake kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse zili m'menemo, zisumbu ndi okhala mommo.
Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,