Masalimo 148:12 - Buku Lopatulika Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu anyamata pamodzi ndi anamwali, inu nkhalamba ndi ana omwe! Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu anyamata ndi anamwali, inu nkhalamba ndi ana omwe. |
M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munakhazikitsa mphamvu, chifukwa cha otsutsana ndi Inu, kuti muwaletse mdani ndi wobwezera chilango.
Ndipo namwali adzasangalala m'masewero, ndi anyamata ndi nkhalamba pamodzi; pakuti ndidzasandutsa kulira kwao kukhale kukondwera, ndipo ndidzatonthoza mitima yao, ndi kuwasangalatsa iwo asiye chisoni chao.
Pakuti ukoma wake ndi waukulu ndithu, ndi kukongola kwake nkwakukulu ndithu! Tirigu adzakometsera anyamata, ndi vinyo watsopano anamwali.
Ndipo pakuyandikira Iye tsono potsetsereka pake paphiri la Azitona, unyinji wonse wa ophunzira anayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mau aakulu, chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu anaziona;